Baibulo
Baibulo
ndi buku
lopatulika
lomwe limakhulupiliwa kuti linapatsidwa kwa anthu kuchokera kwa
Mulungu
. Ilo lagawidwa muzigawo ziwiri- malemba a
Chiheberi
ndi malemba a
Chigriki
. Mabukhu amene amagwiritsidwa ntchito ku
Chiyuda
amatchedwa Tanaka kapena
Baibulo la Chiyunda
. Mabukhu amene amagwiritsidwa ntchito mu
Chikhristu
amatcheda Bukhu Loyera, Mau a Mulungu kapena Baibulo la chi Khristu. Chikhristu chimatenga ma bukhu ena a Baibulo la Chiyuda ku Chipangano cha kale, ngakhale ma bukhu awa amasiyana pa dongosolo lake ndipo ma baibulo ena ali ndi mabukhu owonjezera. baibulo la Chikhristu lili ndi mbali ina ya chiwiri yotchedwa Chipangano cha Tsopano.
Ma bukhu a baibulo amayalidwa mofanana mu zitanthauziro zosiyana siyana. Baibulo la Chikhristu linagawidwa mbali ziwili:
Chipangano cha Kale
ndi
Chipangano cha Tsopano
.
20